ZIKHULUPIRIRO ZA MPINGO WA CONTINUING CHURCH OF GOD.

ZIKHULUPIRIRO   ZA   MPINGO  WA  CONTINUING  CHURCH   OF  GOD.

Mulimbane chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima ( Yuda 3 ).

Chikondi cha pa abale chikhalebe (Ahebri 13:1 ).

Ndipo anali chikhalire mu chiphunzitso  cha Atumwi ( Machitidwe Atumwi 2:42 ) .

Cholinga cha bukhuli ndiko kulongosola zikhulupiriro zimene  membala wa Continuing Church of God amayenera  kutsatira nthawi zonse.   Continuing Church of God inakhazikitsidwa pa 28 Desembala 2012 chifukwa choona kuti Mpingo wa Mulungu sunali kutsatira choonadi cha Baibulo monga osankhidwa ake, posadzipereka   kuchita  choonadi ( 1 Timoteo 3:15 ), mu njira ya Mulungu ( Mateyu 24:14,28:19,20. Yohane 6:2, Zakariya 4:6 -7 ).

Izi zikubweretsa kusiyana pakati pa Mpingo wa Continuing church of God ndi mipingo ina imene ili ndi zikhulupiriro zofanana nafe.

 

ZIPHUNZITSO  ZA  KU  AEFESO  NDI  SMURNA.

Bukhu la Chibvumbulutso ndi  bukhu la Uneneri  “ Chibvumbulutso cha Yesu Khristu,chimene Mulungu anachibvumbulutsira achionetsere akapolo ake, ndizo za zimene zidzachitike posachedwapa ( Chibvumbulutso 1:1 ).

Mumakalata onse aku Chibvumbulutso chaputala 2 ndi 3 tikuyenera kuwamvetsa mwa uneneri chifukwa ali Kunena za zimene zidzachitike mtsogolo osati nthawi imene Yohane anali kulemba.

Tikaona mbiri ya Mpingo wa Chikhristu kupyolera mu makalata seveni aku Chibvumbulutso chaputala 2 ndi 3 ,amationetsera za machitidwe a mbadwo  wa Mpingo owona matsiku ano ( kuti tidziwe zambiri tiyeni tiwerenge Chibvumbulutso chaputala 2 ndi 3.

Mpingo owona sukutchulidwa kuti ndi pulotesitati, katolika,kapena orthodox koma ndi umene umasunga zikhulupiriro  monga momwe Atumwi anali kuchitira.

Anthu ambiri amazitchula kuti ndi Akhristu ndipo amakhulupirira Yesu pamene sakudziwa  kapena kuchita zimene Atumwi anali kukhulupirira.

Baibulo limanena bwino kuti Yesu anayenda mkati mwa Mipingo yonseyi  seveni ( Chibvumbulutso 1 :9 -13 ) zimene zikuonetsera za Mpingo wake mu mbadwo uno.

Seveni  imatathauza za kumaliza, choncho Mipingoyi  imaimirira za Mpingo owona matsiku ano.

Tiyeni tione ziphunzitso za Akhristu oyamba zimene zimatsatiridwa mu nthawi ya Aefeso ndi a Smurna, zimene ife a Continuing Church of God timadzivomereza kudzitsatira.

UBATIZO.

Umachitika pa kumizidwa madzi ndipo sumakhuza ana angono

BAIBULO.

Chipangano Chatsopano ndi Chakale chimagwiritsidwa ntchito ndi Mpingo owona wa ku Asiya minor.

Atumwi  komanso Atsogoleri owona amakhulupirira Mzimu woyera mukunena kwa a binitariyani ndi semi ariyani.

Akhristu oyamba sanali kuchita chikondwerero pa tsiku lawo lobadwa.

KUBADWA MWATSOPANO.

Kumanthathauza za tsiku loukitsidwa osati panthawi imene Munthu  walapa kuleke njira zake zoipa.

Kutchedwa  Bishopu,Abusa sikunali kofunikira kwambiri.

KHIRISIMASI.

Akhristu oyamba sanali kukondwerera pa 25 decembala monga mene ena  amachitira masiku ano, pakuti ichi sichichokera mu Baibulo.

ULAMULIRO WA MPINGO.

Unali kutsatiridwa mwa ndondemeko yoyenera osati  mwachisawawa.

Mapembedzedwe anali kuchitika mwa Uzimu osati mwa chikhalidwe ndi miyambo imene anthu amakopeka  nawo masiku ano.

MDULIDWE.

Unali kuchitidwa ndi Akhristu a ku Nazarete.

Anthu sanali kulapa pamaso pa wa Nsembe poopa chilango.

Chisangalalo cha Akhristu chitapita chiukitso.

Ntchito ya azibusa kunali kulalikira ndipo izi sidzinali kukhudzana ndi mavalidwe awo  kapena kutsatira ma sakaramento.

Atumwi sanali kuchita Esita mwa lamulo.

Masiku oyera a Mulungu anali kusungidwa ndi Akhristu oyamba.

Mulungu anali kutchedwa Atate.

Okhulupirira anali kutsatira Uthenga owona wa Ufumu wa Mulungu komanso anali kumvera Malamulo a Mulungu.

Kumwamba sikunali kunenedwa kukhala Mphoto ya Akhristu.

Mzimu woyera samatchedwa Mulungu kapena munthu ndi Akhristu oyamba

Nyimbo zinali za masalimo osati zomukweza Yesu.

Kulambira mafano pogwiritsa ntchito mtanda sikunali kuloleredwa.

Anali kuphunzitsa kukhazikika kwa moyo  weni weni wa chikhristu .

Yesu anali kutchedwa Mulungu ndi Akhristu owona.

Amalalikira za Ufumu wa Mulungu.

Mkate wokhala ndi chotupitsa unali kutchotsedwa mu nyumba za Akhristu oyamba ndipo Ayuda amachita chimodzi modzi.

Nyengo ya lenti (nyengo yolapa machimo imene Akatolika amchita )siyinali kutsatiridwa.

Mpingo weniweni sumayankhula zokhuzana ndi limbo ( Limbo ndi malo odikirira amene mpingo wa katolika umakhulupirira kuti munthu akamwalira amapita kuyembekedzera .

Mariya anali Mayi ake a Yesu, anadalitsidwa (Luka 1:28) ndipo amatchedwa wodalitsika ( Luka1:48 ) koma Akhristu oyamba sanali kupempherera kudzera mwa iye.

Akhristu oyamba sanali Kutenga mbali pa Usilikali kapena kuchita nawo  Nkhondo.

Yesu Khristu adzalamulira zaka chikwi pa dziko lapansi.

MONASTICISMxxxx

Atumwi anali kuchita Paskha  nthawi zonse pa 14th Mwezi wa Nisan.

Akhristu oyamba sanali kuchita mwambo wa puligatoriyo.

Anali kuphunzitsa za kuuka kwa akufa.

Sabata linali kusungidwa pa tsiku loweruka osati la mulungu.

Chipulumutso chimaperekedwa kwa anthu osankhidwa ( Yuda 3 ).

Munthu adzapatsidwa ulamuliro pa zaka 6000 mu Pulani ya Mulungu.

Atumwi sanali kusunga tsiku la mulungu ngati lopembedza.

Atumwi anali kusunga Malamulo khumi a Mulungu.

Chachikhumi ndi chopereka zimaperekedwa kuti zithandize Utumiki, Mpingo, Anthu osowa, komanso mayendedwe pofalitsa Uthenga wa Ufumu  Mulungu.

Miyambo siyinali kuphatikizidwa ndi Baibulo monga unamwali.

Utatu silinali liwu lolongosola za Mulungu Atate.

Akhristu sanali kudya nyama zodetsedwa.

Mpingo wa Continuing Church of God ukupitiriza kuphunzitsa zimenezi popeza ndi zimene Atumwi oyamba anali kutsatira.

Continuing Church of God  imakhazikika pa Mbiri ya Atumwi  monga  Petro,  Paulo , Yohane, kudzera mupfuko la Polycarp, Polycrates, ndi  Atsogoleri  ena, Ma bishop aku asiya minor, kufikira mbadwo wa chitatu mu chaka cha 135 AD ku Yerusalemu, Komanso  Ma bishop aku Antiokeya monga Serapioni.

Petro anachita zazikulu pakati pa Atumwi ndipo atamwalira Utsogoleri unayenera kupita kwa Mtumwi Yohane osati kwa atsogoleri amene amakhala ku Aroma.

KODI  CHIPHUNZITSO  CHA  KU  FILADEFIYA  ND I CHITI ?

Mpingo wa Mulungu unayamba kutsatira zikhulupiriro zina. Ndipo patapita nthawi choonadi chinayamba kutayidwa ndipo Mpingo unayamba kutaya zambiri zokhudzana ndi choonadi ( Chibvumbulutso 3:1-3 ).

CHOONADI  CHIMENE  CHINABWEDZERETSEDWA  KU  MPINGO  WA  MULUNGU  CHIMENE  CHINATAYIDWA.

 1. Uthenga owona wa ufumu wa Mulungu. ( werengani bukhu lotcedwa  UTHENGA WA UFUMU WA MULUNGU ).
 2. Cholinga cha Mulungu pa Munthu ( werengani bukhu lotchedwa KODI MPINGO WOYAMBA UMAPHUNZITSA KUTI AKHRISTU ADZAKHALA MULUNGU ).
 3. Pulani ya Mulungu kudzera mu Matsiku oyera a Mulungu. ( werengani bukhu lotchedwa KODI MUMAKONDWERERA MATSIKU OYERA A MULUNGU KAPENA MATSIKU ACHIKONDWERERO OCHOKERA KU ZIWANDA ).
 4. Utsogoleri wabwino wa Mpingo ( WERENGANI ZOCHITIRA UMBONI IZI, BAIBULO, POLYCARP,HERBERT .W. ARMSTSTRONG  NDI RODERICK .C. MEREDITH pankhani yokhudzana ndi utsogoleri wa bwino imene Polycarp analembera a Afilipi.
 5. Mulungu ndi Ndani ? ( WERENGANI BUKHU LOTCHEDWA MULUNGU MODZI,ZINTHU ZIWIRI,CIYAMBI CHISANAFIKE ).
 6. Mulungu ndi ndani nanga ndi chifukwa chiani?
 7. Mzimu mwa munthu.

8 Zipatso zoyambirira mu mbadwo uno  ( WERENGANI BUKHU LOTCHEDWA  PENTEKOSTE : IMAPOTSA MACHITIDWE CHAPUTALA 2. )

 1. Chidziwitso choti Meleniyamu ( nyengo ya zaka 1000 zimene Khristu adzalamulire pa dziko lapansi ) ndi chiani.
 2. Choonadi chokuhudzana ndi Mzimu woyera ( WERENGANI BUKHU ILI “ KODI AKHRISTU OYAMBA ANALI KUNENA KUTI MZIMU WOYERA ANALI WAPADERA MU UTATU ).
 3. Panopa Akhristu ndi okondedwa komanso wodalilika. ( WERENGANI ZOKHUDZANA NDI KUBADWANSO, FUNSO LOKHUDZANA NDI SEMATIKI ).
 4. Kubadwanso pa tsiku la chiukitso ( WERENGANI BUKHU LONENA ZA KUBADWANSO NDI FUNSO LA WODALITSIKA).

13.Chidzindikiritso cha Israeli ku thupi.

14.Chidzindikiro cha Israeli chimatithandiza kuti tidziwe uneneri wa Baibulo.

 1. Chachikhumi Chachiwiri ndi Chachitatu (WERENGANI BUKHU LOTCHEDWA : KODI CHCHAKHUMI CHACHITATU NDI CHOFUNIKIRA KUTCHITSATIRA MU NYENGO UNO ).
 2. Chidzindikiro cha Ana a ku Babulo.
 3. Satana wanyenga dziko lonse la pansi ( TSIKU LA KUSALA KUDYA LIMAONETSERA MOYO WA CHIKHRISTU ).
 4. Tikuyenera kukhala osiyana nawo anthu anzathu mu zochitika.

ZINANSO  MWA  ZIKHULUPIRO ZA CONTINUING CHURCH OF GOD.

Mpingo wa Continuing church of God ukuimirira Mpingo wa ku Filadefiya umene zikhulupiriro zake zimachokera mu Baibulo.

Atafa ndi kuuka Yesu. Ziphunzitso ,Machitidwe, Zotiyenereza ndi Miyambo yathu zikuyenera kuchokera ku chiyambi cha Mipingo ya ku yerusalemu ( Machitidwe :2 )  mu 31 AD.  Komanso mwa Okhulupirira a ku A ntiokeya, Asiya minor  monga  Paulo, Petro ndi Yohane ).

Ndipo onse akutsatira ziphunzitsozi  anabalalika kupita Madera ena kumene anakhazikitsa Magulu.

Yesu ananena kuti Mpingo  owona udzakhala kagulu kakangono ka nkhosa ( Luka 12:32 ),kosakondedwa ndi dziko la pansi (Mateyu 10:22 ), ndiponso konzunzidwa ( Mateyu 10:23 ). Iye ananenanso kuti ndi ochepa amene adzatsatira njira yopita ku moyo wosatha mu nthawi ino ( Mateyu 7:14 ,20:16 ).

Mtumwi Yuda ananenanso kuti chiwerengero cha oyera mtima ndi chochepa ( Yuda 4 ) ,pamene Mtumwi Paulo akuti osankhidwa ( Aroma 11:5 ).

Baibulo limanena kuti Mpingo owona suyenera kukhala ndi likulu lake ku mzinda wina uliwonse ( Ahebri 13:14  Mateyu 10:23 ).

Ndi Mipingo yokha ya ku Chibvumbulutso 2 ndi 3 komanso  Mipingo ya Mulungu imene inapitiriza kuwadzindikiritsa anthu za Mpingo owona mu madera onse.

Mu zaka za ma 20 Mpingo owona wa ku Filadefiya unayambika ( Chibvumbulutso 3:7-13 ) ndipo unali kuyendetsedwa ndi wayilesi  yakale ya Mpingo wa Mulungu yotchedwa Worldwide church of God pansi pa utsogoleri wa Herbert .w. Armstrong.

Ngakhale chiphunzitso chake  chinaleka pamene iye anafa koma panabuka abale ena amene anapitiriza kufalitsa maziko a chooonadi (1 Timoteo 3:15 )ndipo akupitiriza mpaka kutha kwa mbadwo uno ( Chibvumbulutso 3:10,11. 12: 14 -17 ).

Mpingo wa Continuing Church of God unakhazikitsidwa ndi cholinga chofuna kudyetsa nkhosa za Ambuye pa dziko lonse la pansi ndi choonadi cheni cheni. Mpingowu uli ndi likulu lake ku California ,America.

BAIBULO.

Baibulo ndi mawu a Mulungu oudziliridwa ndi iye.

Ndipo liri ndi mabuku okwana 66. Mabukhu 39 analembedwa kuchokera mu Chihebri  pamene mabuku 27 analembedwa kuchokera mu Chigiriki.

Mawu a Mulungu anauuziridwa ndipo ali ndi nzeru zotitengera ku chipulumutso ( 1 Timoteo3:15-17. Mateyu 4:4. 2 Petro1: 20,21 ). Mawu ake ndi chooonadi ( Yohane 17:17 ) ndipo sadzasintha nthawi zonse ( Yohane10:35 ).

MULUNGU NDI MZIMU KOMANSO CHIKONDI.

Mulungu ndi mzimu ndipo onse omulambira, amulumbire mu mzimu ndi chooonadi ( Yohane 4:24).

Njira za Mulungu ndi zazitari kuposa njira ndi maganizo athu ( Yesaya 55:9 ).

Mulungu ndi chikondi ( 1 Yohane4:8,18 ), ndipo malamulo khumi amanena za chikondi ndipo kuwaphwanya ndi  kuchimwa.

Mzimu woyera amadzioetsera  mwa Atate,mwana ,ndipo kudzera mwa iwo dziko lapansi limafikiridwa ( 1 Mafumu8:27, Masalmo139:7, Yeremiya 23:24 ).

Pulani ya Mulungu pa munthu yakhazikika pa chikondi.

UMULUNGU

Atate ndi mwana amakwaniritsa umulungu ( Aroma 1:20, Akolose 2;9, Mateyu 11:27 ) ndipo amgwira ntchito kudzera mwa Mzimu woyera. Malemba amanena kuti Mulungu  ndi wosatha  pamodzi ndi mawu ake ( Genesis 1:26, Aefeso 2:19, 3:14,15. Yohane 1:1,14. ) wakuonjezera okhulupirira ( Ahebri2:10,11, 1 Yohane3:1,2, Aefeso 3:14,15 akukhala monga Yesu Khristu ( Aroma 8:29 9) amene ndi Mulungu ( Yohane 1:1-3, 20:28-29, Akolose2:9 ).

Mzimu woyera Sali wapadera koma amaperekedwa kwa iye amene walapa ndi kubatizidwa.

UTSOGOLERI WA MU BAIBULO.

Yesu anati Atate wanga ali wamkulu kuposa ine ( Yohane 14 :28 ) pamene Paulo nati Mutu wa khristu  ndi Mulungu ( 1 Akorinto 11:3 ).

Wolamulira chilengedwe chonse ndi Mulungu atate.

Khristu ndi mutu wa Mpingo ( Aefeso 5:23 ) ndi mawu (Yohane 1:14 ) ndipo palibe mtsogoleri amene ayenera kutsutsana ndi mawu a Mulungu ( Marko12:13 – 27  Machitidwe atumwi 5:29 )

Ndondoneko za utsogoleri zikuyankhulidwa mu chipangano chatsopano ( 1 Akorinto 12:28 ). Izi zikusonyeza kuti ndizo zoyenera ku Mpingo ( Aefeso 4:11 -16] .izi zimachitika mwa ndondomeko kuyambira pa Atumwi a Yesu ,kenako Aneneri ,kenako Alaliki,kenako Abusa ,kenako Aphunzitsi

[Aefeso 4;11].  Kuchokera  panthawi  ya Pentekoste  [Machitidwe atumwi 2; 1-4, ) Atumwi  akhala akusankhidwa  kudzera pa kuyikidwa manja ndi Mzimu woyera ,kuyamba ndi Atumwi[Machitidwe 9; 17,2 Timoteo 1;6 ndi ena onse amaikidwa  manja ngati mbali imodzi ya Utumiki.

Akhristu ayenera kumvera atsogoleri awo mwa Ambuye[ahebri13;7,17].

Atsogoleri  ayenera kukhala ogwira mawu a Baibulo ndikuwatsata [1 Timoteo 3;1-12, Ahebri 13;17,Mateyu20;25-28]

AKHRISTU AYENERA KUKHALA MU CHIKONDI CHAKE

Mulungu ndi chikondi [Yohane3;16, 1 Yohane4;8-18]ndipo Malamulo ake [Mateyu22;37-40]ndi njira  moyo[ Yakobo2;8-11,1 Yohane5;3]’’Mwa izi tidziwa kuti mukonda iye ngati musunga Malamulo ake ,iye wakunena kuti amudziwa iye koma osasunga malamulo ake ndi wabodza

1 Yohane2;3-6

Akhristu ayenera kusanzira khristu  [1 Akorinto11;1].kuwonjenzera pa  kusunga malamulo,ndi kupereka.

Akhristu ayenera kupemphera nthawi zonse .[1Atesalonika 5:17 },kuwerenga mawu a Mulungu { Machitidwe 17: 11. 2 Timoteo2 :15 }, kulingalira mawu ake {  Afilipi 4:18 }, kusala kudya { Mateyu 6:16 -17 }.

Akhristu ayenera kukhala a chikondi ( Mateyu 22:36-40 ) ndi chifundo ( Luka 6:36 ).

Ma uthenga onse mu baibulo amanena za chikondi pa mulungu komanso pa wina ndi nzake ( Marko 12: 30-31).

Kupatula pa chili chonse chimene munthu amachita,chikondi ndicho chofunikira kuposa zonse ( 1 Akorinto 13:13 ).

UCHIMO NDI LAMULO LA MULUNGU.

Baibulo limaphunzitsa kuti tchimo ndiko kuphwanya lamulo ( 1 Yohane 3:4 ).

Yesu amasunga ndi kunena za malamulo khumi ( Eksodo 20:1-17, Deutoronomo 4: 13, 10:4 ) ngakhale mu chipangano chatsopano ( Mateyu 5:17 -48, 12: 12 ).

Yesu anakwaniritsa ulosi onena kuti iye adzalemekeza  ndi kukweza malamulo ( Yesaya 42:21 ). Mu chipangano chatsopano Akhristu anali kusunga malamulo ndipo izi anali kuchita anali Akhristu eni eni osankhidwa amene amakhulupirira Yesu  (Chibvumbulutso 14:12 )

CHIKHULUPIRIRO, KULAPA ,  KULANDIRA YESU, KULUNGAMITSIDWA, KUBWEDZERETSEDWA, UBATIZO.

Kupatula kuitanidwa ndi Mulungu ( Yohane 6:44 )chinthu cofunikira ndiko kumva  chifukwa chikhulupiriro chimadza pa kumva mawu a Mulungu ( Aroma 10:17 ).

Munthu amakhulupirira pamene wamva mawu a Mulungu  ( Machitidwe 8:37, 24:14 )

Anthu amene akhazikika mu chikhulupiriro pakumvetsa mawu a Mulungu ndi amene ayenera kubatizidwa kukhala akhristu owona ( 1 Akorinto 7:14 ). Pamene wabvomereza uthenga wa Yesu umakupangitsa kulapa zintchito zako za kale zonyansa ndikuyamba kukhulupirira Mulungu ( Ahebri 6 ;1 ) pakusiya chikhalidwe choyamba chotsutsana ndi Malamulo a Mulungu ( 1 Akorinto 6:6-11 ).

Kubatizidwa mu dzina la Yesu kuloza ku chikhululukiro cha machimo ( Machitidwe 2:38 ) ndi kusanjikidwa kwa manja ( Ahebri 6:2, Machitidwe 8:14 – 17 ), ndipo udzalandira mphatso za mzimu woyera  ( Machitidwe 2:38 ).

Akhristu amalungamitsidwa kudzera mu mwazi wake (Aroma 5:9 ) ndipo amabwedzeretedwa kwa Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake ( Aroma 5:10 ).

Ubatizo umachitika kupyolersa mu madzi. Mu chigriki mawu oti ubatizo amathanthauza kumizidwa ndipo izi zimatsindikiza za kudzipereka kwathu kwa Mulungu ( Aroma 6 :3 -13 ).

Chipangano chatsopano chimalongosola kuti Mzimu woyera unali kuperekedwa kwa amene wabatizidwa kudzera mukutsanjikidwa kwa manja ndi Atumiki Akhristu monga Atumwi, Akulu a mpingo ( Machitidwe 8:17, 9:17, 19:6,  2 Timoteo 1:6 ).

Mulungu amadzionetsera yekha kwa akhristu okondeka ake, kudzera mwa Mzimu woyera  ( 1 Yohane 5:1, 1 Petro1:3 )ndipo patapita nthawi ya kukulanso kwa moyo wa Uzimu, Akhristu adzabadwanso mwatsopano pa tsiku la chiukitso ( Yohane 3: 5 -7 ) monga khristu (Aroma 1:4,5 ).

UMULUNGU NDI CHIKHRISTU CHOONA .

Akhristu amakhulupirira mwa Atate, Mwana ndi Mzimu woyera ndipo Atate ndi Mwana amapanga Umulungu.

Kuli Mulungu modzi  ( Marko 12:29, Yohane 17:11. 1 Akorinto 8;4 )amene amaonetsa umulungu wa banja losatha mwa awiri amene ndi Mulungu Atate ndi Mawu  ( Geenesis 1:26, Aefeso2:19, Yohane 1:1,14, Mateyu 11: 27, Yohane 17: 10,11. Ahebri 2:10,11. 1 Yohane3:1,2,. Aefeso3:14,15.

Yesu ( mawu ndi mwana wa mulungu ) ndi Atate ndi Mulungu.

Mzimu woyera amachokera kwa Mulungu ( 1 Mafumu 8:27 , Masalmo 139 :7 , Yeremiya 23:24,) ndipo amaperekedwa kwa onse alapa machimo awo, nabatizidwa ( Machitidwe 2:38,39 ). Mzimu woyera ndi wa mphamvu ( Machitidwe 1:8 , 2 Timoteo 1:6,7 ) ndipo amathandiza okhulupirira kugonjetsa choipa ( Aroma 12:21, Chibvumbulutso2:26,27. )namawatsogolera ku moyo wosatha ( Afilipi 3:12, Aroma 6:23,

Mzimu wa Mulungu umabweretsa kusiyanitsa pakati pa khristu owona ndi wabodza ( Aroma8:9 ).

Ambiri amene amaganiza kuti ndi Akhristu koma sasunga malamulo oterowo  Sali Akhristundipo Sali mu chikondi chake  ( Mateyu 7:21-23. Luka 13:24-27, Yohane 15:9,10. 1 Yohane 2 :6 )

UTHENGA WA KHRISTU WA UFUMU WA MULUNGU.

Uthenga wa ufumu wa Mulungu unali uthenga umene Yesu ( Marko 1:14, Luka 4:43, Mateyu 9:35, ) ndi ophunzira ake anali kulalikira ( Machitidwe 19:8, 20:25, 28:23,30,31. 2 Petro1:10,11.).

Uthengawu unali kukhunzana ndi kulapa machimo , imfa ya khristu, njira ya mulungu ya ku moyo wosatha ndi kubwera kwa ufumu wa Mulungu (Marko 1: 14,15. Machitidwe 8:12, 17:7, 28:30,31. Chibvumbulutso 2: 26,27. ) kumene kudzabweretsa chimariziro cha pansi pano komanso kutha kwa maulamuliro ndi mphamvu zonse.

Uthengawu ukunena za choonadi kuti Mulungu adzapereka chipulumutso kwa onse (Luka3:6  Yohane3:16,17. 12:32,47, Yesaya  6: 9 -11  ). Uthenga wa ufumu wa Mulungu umakamba za Yesu, Mpingo woyamba komanso  Chipulumutso.

Ife a continuing church of God tikupitiriza ntchito ya kulalikira chooonadi mpaka kubwera kwa Yesu.

CHIPULUMUTSO KUDZERA MU DZINA LA YESU,MWA  CHISOMO KUDZERA CHIKHULUPIRIRO NDI KUBWERA KWAKE.

Palibe dzina lina pansi pa nthambo limene  lapatsidwa kwa munthu limene  tiyenera kupulumutsidwa nawo ( Machitidwe 4:10,12 ).

Yesu anati ine ndine njira,choonadi ndi moyo, palibe adza kwa Atate osadzera mwa ine (Yohane 14:6 ).

Pakuti muli opulumutsidwa mwa  chisomo ,chakuchitika mwa chikhulupiriro ndipo ichi sichichokera kwa inu, koma chili mphatso ya Mulungu , chotsachokera kwa munthu kuti wina adzitamandire ( Aefeso2:8,9. ). Iyi ili mphatso ya Mulungu kudzera mu chikhulupiriro mwa Yesu khristu ( Tito 3:5, 2 Akorinto 2: 15, Aroma 5: 10 ).

Mulungu ndi wa chifundo ( Eksodo 34:6, Luka 6:36 ) amene akufuna tonse tipulumutsidwe ( 1 Timoteo 2:4 ) koma chifukwa cha zovuta zina ndi ochepa okha amene adzapeze chipulumutso ( Mateyu 7:14, Luka 13:23,24. Aroma11:6,7 2 Akorinto 4:4 ).

Munthu akalapa ndi kubatizidwa, Mulungu amamulungamitsa munthuyo pakutchoka ku machimo ake akale ndipo amayamba ulendo wa Chipulumutso ( 2 Petro 3:18 ) ndipo Khristu amakhala mwa iye ( Agalatiya 2:20 ).

Chipulumutso cha Akhristu chidzakwaniritsidwa pa tsiku la chiukitso ( 1 Akorinto 15: 50-54 ).

Khristu anaperekedwa kuti asenze machismo athu onse natipatsa chiyembekezo cha chipulumutso ( Ahebri 9:28 ).

CHIKONDI NDI CHIPULUMUTSO KWA ANTHU A MITUNDU YONSE.

Kudana chifukwa cha kusiyana mitundu ndi kulakwitsa.

Baibulo siliri kutiphunzitsa kuti kuli mtundu wopambana kuposa unzake ayi  koma limalamulira kukondana wina ndi nzake monga uzikondera iwe mwini ( Levitiko 19:18, Mateyu 22:39, Machitidwe 17: 24 -29 ).

Yesu anabwera kudzapereka chimwemwe kwa wina aliyense ( Luka 2:10 ) ndipo chipulumutso chinaperekedwa kwa ulere ,kwa Ayuda komanso kwa Amitundu ( Machitidwe 10 :34,35. Aroma 10:12,12. Jowelo 2:32 ).

Ndi cholinga cha Mulungu ndiko kupulumutsa anthu a mitundu yonse ndi zilankhulo zonse ( Chibvumbulutso  7:9 ). Chikondi cha Khristu chiyenera kuonekera  kwa anthu a mitundu yonse ( Aroma 13:10, Luka 10: 30 -37 ).

Mulungu wathu ndi Mulungu wopulumutsa ( Masalmo 68 :20 ) ndipo thupi liri lonse lidzaona chipulumutso cha Mulungu ( Luka 3:6 )

BAIBULO LIMANENA CHIANI ZA DZINA LA MPINGO.

Kunena za Mpingo owona mu chipangano chatsopano unali kuchedwa  ‘Mpingo wa Mulungu “ , nkhaniyi ikufotokozedwa bwino  mu mabukhu awa  (  Machitidwe 20:28, 1 Akorinto1:2 , 10:32, 11:16,22, 15:9, 2 Akorinto 1:1, Agalatiya 1:13, 1 Atesalonika 2:14, 2 Atesalonika 1:4, 1 Timoteo 3:5,15 ).

Mu mbiri yonse ya Mpingo, Mpingo owona umagwiritsa ntchito dzina loti  “ MPINGO WA MULUNGU KAPENA MPINGO WA KHRISTU “. ( Aroma 16 :16 , Yohane 17:12, ).

Choncho Mpingo wa Continuing Church of God  ukupitiriza kusunga dzinali , chifukwa ndi Mpingo umene ukupezeka mu bukhu la Chibvumbulutso ndipo umakhazikika pa chikondi cha pa Abale ( Felidefiya ).

SABATA, MELENIYAMU  NDI  MATSIKU OYERA  A  MULUNGU .

Sabata ndi tsiku loweruka ( Genesis 2:2,3. Eksodo 20:8-11, Ahebri 4:4,9 ).

Baibulo limanena kuti Yesu khristu (Luka 4:16, 6:6, 13:10, Marko 6:2,) Atumwi ( Machitidwe17:2, 18:4 ) anali kusunga lamulo la sabata.

Yesu anati iye ndiye Mbuye wa sabata ( Marko2:28 ) ndipo tsiku la Ambuye ndilo sabata limene likubwera pa tsiku la chisanu ndi chiwiri.

Pakuti ichi ndi chidzindikiro pakati pa Munthu ndi Mulungu ( Eksodo 31:13 ).

Tsiku la chisanu ndi chiwiri ndilo lopuma anthu ake ( Ahebri 4:9 ). Sabata limatiunikiritsa za kulamulira kwa Yesu ( Ahebri 4:1-4, 2 Petro 3:8, Chibvumbulutso 20:4-6 ).

Yesu adzalamulira zaka 1000 pa dziko lapansi pamodzi ndi okhulupirira ( Chibvumbulutso 5:10. 20:4-6 ). Ndipo ulamuliro uwu wa zaka 1000 baibulo limanena kuti udzakhala wodabwitsa ( Yesaya 2:, 9: ,11:1-11, 35: 1-9, Ezekieli 34:21-29, Mika 4:1-4, Machitidwe 3:9-21, ) ndipo okhulupirira adzalamulirira ndi Khristu ( Chibvumbulutso 20:1-6 ).

Panthawi imeneyo satana woipayo adzamangidwa ( Chibvumbulutso 20:1-6 ) ndipo idzakhala nthawi yopuma  ndi kukhala nazo zochuluka.

Sabata limasungidwa kuyambira kulowa kwa dzuwa kwa lachisanu mpaka kulowa kwa dzuwa kwa loweruka.

ZIKONDWERERERO ZA MATSIKU OYERA A MULUNGU : Angakhale kuti zinthu zina zinasintha mene ana Aisraeli  anali kuchitira koma Akhristu oyamba anali kupitiriza kuchita zikondwerero za Matsiku oyera a Mulungu  ( Levitiko 23: ).

PASKHA

Imanena za nsembe imene Yesu anadzipereka “ Mwana wa nkhosa wa Mulungu amene atchotsa machimo a dziko lapansi ( Yohane 1:29 ) .

Yesu anali kuchita paskha chaka ndi chaka ( Mateyu 26:18, Marko 14:14, Luka 2:41,42. 22:15 ) iye anafa pa paskha ( Luka 22:15 ) ndipo anadzipereka nsembe malo mwa ife ( 1 Akorinto 5:7 ).

Yesu anasintha zina zokhunzana ndi paskha powonjezera chidzindikiro cha Vinyo ndi Mkate wopanda chotupitsa ( Mateyu 26: 17, 26-28. 1 Akorinto 11:23-26 ) Kutsuka mapazi ( Yohane 13: 1-17 ). Izi zinali kuchitika chaka ndi chaka ( Eksodo 13:10 ).

Pamene tichita paskha timalalikira za imfa ya Yesu khristu ( 1 Akorinto 11:27 ) imene imabwedzeretsa ubale wathu ndi Mulungu.

Yesu napereka moyo wake pa chipulumutso cha moyo wathu ( Yohane3:16,17. Ahebri  5: 5-11 ) ndipo imfa yake imatiphunzitsa kuti sityenera kulora tchimo kulalamulira mu thupi lathu ( Aroma 6: 3-12 ).

TSIKU LA MKATE WOPANDA CHOTUPITSA.

Limachitika ikatha paskha, limene limanena za kuyeretsedwa ku machimo  athu kudzera pa kudzipereka nsembe kwa Yesu ( 2 Petro 1:9-11 ) ndikuchitira umboni  za kulekana ndi choipayo ( 1 Akorinto 5: 6-13 ).

Paulo mtumwi analemba  “ Pakuti chifukwa chake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale,kapena chotupitsa cha dumbo ndi kuipa mtima,koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima ndi choonadi “ ( 1 Akorinto 5:8 ).

PENTEKOSTE.

Pentekoste imakamba za chikondwerero cha kukolora kwa zipatso zoyambirira  mu chipangano chakale( Eksodo 23:16 ) pamene mu chipangano chatsopano  ndiko kuyamba kwa mpingo ( Machitidwe 2: 1 -4 ).

Pentekoste imanena kuti Akhristu ndi mbewu yoyambirira ya Mulungu ( Aroma8:23, 11:16. 1 Akorinto 15:20-23, Yakobo 1: 18 ).

Antchito ndi ochepa  ( Mateyu 9: 37-38 ) .Awa ndi Akhristu amene amatsata mwana wa nkhosa kuli konse akupita ndipo ndiwo osankhidwa (    Chibvumbulutso 14:4,5 ).

CHIKONDWERERO CHA MALIPENGA.

Uku ndi kuimbidwa kwa Malipenga Seveni mu bukhu la Chibvumbulutso onena za zimene zidzachitike pa tsiku la Ambuye ( Chibvumbulutso 8: , 9: , 11:15-18, 15:1-8, 16:1-21, 19: 1-20 ).

Lipenga lotsiriza limasonyeza za kuuka kwa Okhulupirira “ Pakuti lipenga lidzalira ndipo akufa adzaukitsidwa,osabvunda ndipo ife tidzasandulika ( 1 Akorinti 15:52 ).

Pakuti Ambuye adzatsika kumwamba mwini yekha ndi mpfuu ndi mawu Ngelo wamkulu ndi lipenga la Mulungu, ndipo akufa mwa Ambuye adzauka koyamba ( 1 Atesalonika 4:16 ).

Chaka chopumula chimayamba ndi tsiku loyera  ( Levitiko 25:1-7, Deutoronomo 15: 7-11 ).

TSIKU LA KUSALA.

Tsikuli limationetsera za kufooka kwathu ndi kufunikira  kwa kukhala chifupi ndi Mulungu. (  Machitidwe 27:9,  Yesaya 58: 5,11. ). Limationetsera kuti Yesu anadzipereka nsembe chifukwa machimo athu  ( 1 Yohane 4: 9,10.  Levitiko16: 15,16. ) komanso ambadwo ulinkudza ( Mateyu 12:32, Marko 10:20, Luka 18:30, Machitidwe 3:21 ).

Limatithandizira kudziwa kuti satana ali ndi gawo pa kuchimwa kwa munthu ndipo iye adzalangidwa pa kumangidwa kwa zaka chikwi ( Chibvumbulutso 20:1-3, Levitiko 16: 20 -26, Yesaya 14:12-16 ).

CHIKONDWERERO  CHA  MSONKHANO  WA  MISASA.

( Levitiko 23: 33-39 )

Tsikuli limakamba za mene  okhulupirira adzalamulire mu Ufumu umene ulikubwera  (  Chibvumbulutso 20;4-5 )ndi Yesu Khristu ( Zekariya 14:, Mateyu 9:37,38. 13:1-30, Luka 12:32, Yohane 7: 6-14, Chibvumbulutso 5:10. 11:15, 12:9 ) mu Paradizo pa tsiku lakubwera Ambuye ndi chitsautso chachikulu ( Mateyu 24:21-31, Deutoronomo 31: 10-13 ).

TSIKU LALIKULU LOTSIRIZA.

Tsikuli limanena kuti onse amene anakhala ndi moyo adzakhala ndi mwayi wa Chipulumutso  ( Yohane 7:37-38, Yesaya 52:10, 13-15, 65:20 ,Luka 3:6 ) mwayi umene ambiri adzaulandira ( Yohane 7:37-39, Aroma 11;25-26. Ezekieli 37:11-14, Ahebri 9:27-28 ).

Yohane mtumwi analemba  “koma pa tsiku lomaliza, lalikulu la phwando  Yesu anaimirira napfuula ndi kunena kuti ngati pali wina akumva ludzu adzekwa ine namwe. Iye wakukhulupirira monga chilembo chinena “ Mitsinje ya madzi a moyo idzayenda kutuluka mkati mwake ( Yohane7:37-38 ).

Mbiri imanena kuti otsatira Yesu khristu oyamba  anali kusunga sabata ndi Matsiku Oyera  onse a zikondwerero zonse tadzitchulazi monga mwa Baibulo.

Pakutsatira matsiku amenewa Akhristu amatha kumvetsetsetsa pulani ya Mulungu ya chipulumutso komanso zoyenera kutsatira zimene zingatibweretsere chipulumutso.

Zikondwerero za mu Baibulo zimatidzindikiritsa kuti Khristu anadzipereka nsembe ( 1 Akorinto 5:7 ) ndipo akhristu ayenera kukhala opanda chinyengo chili chonse ( Luka 12:1 , 1 Akorinto 5:6-13 ).

Palinso mbadwo umene ulinkudza ( Machitidwe 3:21, Mateyu 12:32, Yohane7: 37,39. 12: 47-48, Aroma 10: 10-21 ).

CHACHIKHUMI NDI CHOPEREKA.

Baibulo limaphunzitsa kuti chachikhumi chonse  ndi cha Yehova ( Levitiko 27:30 ), Akhristu amene anali kutsatira Yesu anali kutsatira ndi kuchita zimene iye ananena zokhudzana ndi chachikhumi ( Mateyu23:23 ), Paulo mtumwi ( 1 Akorinto 9:1-14 ).

Munthawi ya chipangano chakale chachikhumi cinali kuperekedwa kwa Ansembe ndipo izi zinasinthika mu nthawi ya utumiki wa Yesu ( Ahebri 7:1-12 ).

Kudzera  mu chachikhumi ndi chopereka Akhristu amatumikira Mulungu pa kuthandiza kulalikidwa kwa Uthenga ( 1 Akorinto 9:9 ), kuthandiza ma Utumiki ( 1 Timoteo 5:17,18. ) Mpingo ( 2 Akorinto 9:6 -14 ) kupezeka ndi kuchitika kwa zikondwerero zake ( Machitidwe 18:21, Deutoronomo 14:22-26 ) Zofunikira za Mpingo ( 1 Akorinto 12:28, 2 Akorinto 9;6-14 ) Zofunika za anthu osowa ( Agalatiya 2:10, Deutoronomo 26: 12-15. 2 Akorinto 9: 6-14 ).

IMFA.

Kwaikidwa kwa munthu kufa kamodzi ( Ahebri 9:27 ).

Pakuti onse anachimwa ( Aroma 3:23 )

Mphoto yake uchimo ndi imfa ( Aroma 6:23 ).

KUUKA KATATU, KUWERUZIDWA KATATU

(1 Akorinto 15:22-23 )

Baibulo limatiphunzitsa kuti kudzakhala  kuukitsidwa katatu.

 1. Okhulupirira ( oyera mtima ) pamene Yesu adzabwere ( Chibvumbulutso 20: 5-6, Yohane 5:24, 1 Atesalonika 4:16,17. 1 Akorinto 15: 51-53 ).
 2. Kuukitsidwa kwa ena. ( Chibvumbulutso 20:5a, 11-12, Yohane 5:25, Mateyu 11: 23-24 ).
 3. Kuukitsidwa kwa anthu oyipa amene anafa kale kale ( Chibvumbulutso 20:13,14, Yesaya 65: 20 -23 ).

ZIWERUZO  ZITATU.

Baibulo limakamba zaziweruzoo zitatu “ chiweruzo chilibe chifundo  ( Yohane 2:13 ).

Mu moyo uno akristu amaweruidwa ( 1 Petro 4:17 ).

Chiweruzo chachiwiri chidzachitika pomaliza pa zaka chikwi zimene khristu adzalamulira pamodzi ndi oyera mtima ( Chibvumbulutso 20:4-6 ).

Patatha izi molumikizana ndi zaka 1000 ( Yesaya 65:20 ) chiweruziro chotsiriza chidzafika ndipo Nyanja  idzapereka akufa anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo ndipo anaweruzidwa monga mwa ntchito zawo ( Chibvumbulutso 20: 13,14 ). Ndipo ngati wina sanapezeke mu bukhu la moyo,adzaponyedwa mu nganjo ya moto ( Chibvumbulutso 20:15, Malaki4:1-3 ,Masalmo 37:38 ). Ndipo amene mayina awo adzapezeke mu bukhu la moyo adzalandira thupi lina komanso azakhala mu banja la Mulungu.

KUMENE  MUNTHU  AZAKHALA     .

Baibulo limanena kuti Yesu anatenga thupi la munthu ( Afilipi 2 : 7 ) kuti munthu akhale mbale wake mu banja la Mulungu. ( Aroma 8:29 , Aefeso 3:14 -19 ).

Yesu anapemphera nati : Ndipo ulemerero umene mwandipatsa ine, ndapatsa iwo: kuti akhale amodzi monga ife tili amodzi. Ine mwa iwo ndi inu mwa ine,kuti akhale angwiro mwa modzi, potero kuti dziko lapansi likadzindikire kuti inu munandituma ine,nimuwakonda iwo monga munandikonda ine litsanakhazikike dziko lapansi  ( Yohane 17:22-23 ) “Kodi mpingo woyamba umaphunzitsa kuti Akhristu adzakhala Mulungu? “

Koma Akhristu oitanidwa amene adzapirire kufikira chimaliziro, iwo adzalandira mphoto mu ufumu wa Mulungu umene udzakhazikitsidwe pa dziko ( Yohane 14:1-3, Chibvumbulutso 3:21, 20:4-6, Mateyu 5:5 Chibvumbulutso 2:26,27. 5:10, Danieli 2:44 ).

CHITSAUTSO CHACHIKULU, CHITETEZO , TSIKU LA AMBUYE, KUBWERA KWA YESU.

Yesu anati “ Pakuti padzakhala masautso akulu,monga sipadakhalenso  otero kuyambira chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde ndipo sipazakhalanso. 22. Ndipo akadaleka kufupikitsa masiku awo sakadapulumuka munthu aliyense. Koma chifukwa cha osankhidwawo, masiku awo adzafupikitsidwa ( Mateyu 24:21,22 ).

Baibulo limanena kuti Mulungu ali kulonjeza kuteteza okhulupirira owona amene adzasonkhana malo amodzi munyengo yoyetsedwayi  ( Zefaniya 2:1-3 ,Joweli 2:16,17. Yeremiya 4:5,6,. Chibvumbulutso 3:7-10 ).

Koma lonjezoli  silinaperekedwe kwa Akhristu onse ( Chibvumbulutso 11:15, 20:4. Luka 21:36 ).

Pali tsiku la Ambuye limene limatha ndi chaka chimodzi ( Yesaya 34:8, ) mpaka kubwera kwa Yesu Khristu  (Yoweli  2 : 30,31. Mateyu 24:29-31, ) ndi kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu ( Chibvumbulutso 11:15, 20:4, 1 Atesalonika 4:13-18  ).

Tsiku la Ambuye lidzabweretsa chionongeko cha ochimwa ( 2 Petro 3:10-12 ) oipa ku ng’anjo ya moto ( Chibvumbulutso 20: 14,15 )

OKANA KHRISTU SICHIROMBO CHA MU NYANJA

Okana khristu ndi atsogoleri a zipembedzo ( 2 Yohane  7, 1 Yohane2:18, 2:22, 4:3 ).

Baibulu limanena kuti aneneri onyenga alowa mu dziko amenewa ndiwo okana khristu ( 1 Yohane 4:1,3,  3: 18-22 ),

Okana khristu omaliza ndi zirombo ziwiri zimene zikunenadwa ku Chibvumbulutso 13;11-17, amene amatchedwa Aneneri onyenga ( Chibvumbulutso 16:13 , 19:20 , 20:10 ). Chirombo china mu Chibvumbulutso 13:1-10 “ chirombo cha mu Nyanja” monga ananenera  Daniel chaputala 11:

OSATI WA DZIKO LAPANSI.

Yesu anati Ufumu wanga si wa dziko lapansi ( Yohane 18:36 , Lluka 3:14, ), Mpingo wa Mulungu ndi mamembala ake sayenera kutenga mbali pa nkhondo yochitika mu dziko kapena kapena kuonera mafilimu a nkhondo.

Paulo mtumwi anati Ndife akazembe a khristu ( 2 Akorinto5:20,Aefeso 6:20 ) . Petro mtumwi  anati ndife mtundu wosankhika,anthu a  iye mwini amene anatiitana tilalikire za iye mwini ( 1 Petro 2:9 ).

Baibulo limanena kuti dziko lapansi linanyengedwa ndi  satana woipayo ( Chibvumbulutso 12: 9 ) choncho anthu a Mulungu ayenera kudzipatula ku zinthu za dziko lapansi ( Yohane 15:19, 2 Akorinto 6:14-17 Yakobo 4:4, Chibvumbulutso 18:4 ).

Popeza Akhristu ndife Akazembe  uwu ndi udindo wathu kupewa za dziko lapansi ( Machitidwe 4:18-20, 5:26-31 )

Ndi udindo wathu kuti sitiyenera kutenga mbali pa zisankho za dziko kapena kulowa usilikali kapena kuchita ndale.

Ndi udindo wa akhristu kumvera ndi kupempherera atsogoleri a dziko, kulipira msonkho ( 1Timoteo 2:1-3. 1 Petro 2:13-17, Mateyu 22:17-21).

Ngati pali kulimbana pakati pa malamulo a Mulungu ndi malamulo a munthu “ Tiyenera kumvera Mulungu koposa ulamuliro wa munthu ( Machitidwe 5:29 )

KUGWA .

Kugwa uku ndi kwa anthu amene anayamba  moyo wa chikhristu kale ( 2 Atesalonika 2:3, 1 Timoteo 4:1  werengani bukhu lotchedwa Kugwa ).

UKWATI WA BAIBULO.

Yesu anati ukwati ndi pakati pa mwamuna modzi ndi mkazi modzi ( Marko 10: 6-9 ) ndipo umakhala wamuyaya ( Mateyu19:3-9, 2 Akorinto 7:39 )

Baibulo limalimbikitsa kugonana muli banja osati musanamange banja  ( 1 Akorinto 6:19, 7: 5 ). Baibulo limaletsa kugonana kuli konse ngati anthu Sali m’banja ( Eksodo 20:14, Aroma 1:24-32, Levitiko 18:22, 20:13, Deutoronomo 23:17-18, 27:21 ,Eksodo 20:17 ,Levitiko 18:6-23 ,20:15,16. Mateyu 5:27,28. 1 Akorinto 6:9-11, ).

Anthu amene amachita chigololo, chiwerewere,kugonana amuna kapena akazi okha okha  Sali oloredwa kutenga  mbali panthawi ya mapemphero kapena kutchedwa membala wa Continuing church of God  chifukwa sanatembenuke mu choonadi.

Banja limapereka chinthunzi nthunzi  cha ubwenzi wa Yesu ndi mpingo ( Aefeso 5:22-32 ).

Mulungu amadana ndi kulekana mu banja ( Malaki 2:16 ).

Chipangano chatsopano chimalora kulekana ngati pali Chimo la chigololo ( Mateyu 5:31-32,  19:3-9, 1 Akorinto 7: )

Musakhale omangidwa gori ndi osakhulupirira. Pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama kapena mdima uyanjana bwanji ndi kuunika. Ndipo khristu abvomerezana bwanji ndi  beliyali,kapena okhululupirira ali nawo bwanji gawo ndi wosakhulupirira ( 2 Akorinto 6:14 -16, 7:39 ).

Mpingo umatsutsa ukwati wa pakati pa okhulupirira ndi wosakhulupirira ( Eksodo 22:16 ).

CHOLINGA  CHA  MPINGO.

Cholinga cha Mpingo ndiko kukweza ndi kulalikira uthenga wa Khristu wa ufumu wa Mulungu ( Mateyu 24:14 ).

MFUNDO  SEVENI  ZA CHOLINGA CHA MPINGO WA CONTINUING CHURCH OF GOD.

 1. Kulalikira uthenga wa ufumu wa Mulungu ( Mateyu 24:14 ) ,Chipulumutso mwa Yesu khristu ( Mateyu 28:19,20 Yohane 6: 29, Machitidwe4:10,12, Aroma1:13 ). Ndikupitiriza kuphunzitsa anthu  akhale mu chiphunzitso.( 1 Timoteo 4: 16 ).
 2. Kuchenjeza za Uneneri  matsiku otsiriza ,kubwera kwa  chitsautso chachikulu ku mbadwo wa Yakobo ndi mibadwo ya nthawi ino ( Mateyu 24: 4-52,  Ezekieli 3: ).
 3. Kulalikira za chikondi cha pa abale ( Chibvumbulutso 3: 7-12, Yakobo 2:8,  Yohane 13:35, Ahebri 13:1 ),  kudyetsa nkhosa ( Mateyu28:19,20 , kulimbikitsa umodzi pakati pa abale ( Joweli 1:14, 2:15,16 Zefaniya 2:1-3, Yeremiya 4:5,6 , Chibvumbulutso 3:7 -10 ) kulimbikitsa za kukula mu chisomo ndi chidziwitso cha Yesu khristu ( 2 Petro 3:18 ).
 4. Kuphunzitsa akhristu kukhala chitsanzo ( Mateyu 5:14-16 , 1 Atesalonika 1:7 ), komanso mboni kwa akhristu azathu ndi dziko lapansi ( Mateyu 24:14  Danieli 11:32,33 ).
 5. Kuphunzira ndi kuchitira umboni za malamulo a Yesu pamene ticheza ndi anthu ( Yohane 13:35 ,15:14 ).
 6. Kubwezeretsa ndi kuphunzitsa zambiri za choonadi cha khristu.
 7. Kuphunzitsa kuti Akhristu ayenera kutsogozedwa ndi mzimu woyera , ayenera kuwonetsera chikondi , chifundo, chikhulupiriro, chilungamo , chiweruziro komanso zipatso zonse za mzimu woyera  ( 1 Akorinto 13: 1-14 ) Mateyu 23:23 ,Agalatiya 5:22-25 ).

Kuphunzitsa choonadi ndi chikondi cha mawu a Mulungu ndi kwa onse oitanidwa ( Mateyu 28: 19-20 ).  Izi ndi zolinga za Mpingo wa Continuing Church of God.

KALENDALA  WA  MATSIKU  OYERA  A  MULUNGU  2019.

PASKHA          =                                           19  EPULO 2019.

MKATE OPANDA CHOTUPITSA      =         20 MPAKA 26 EPULO 2019.

PENTEKOSTE            =                             9 JUNI 2019.

CHIKONDWERERO CHA MALIPENGA  =    30 SEPITEMBALA  2019.

TSIKU LA KUSALA KUDYA   =         9 OKOTOBALA 2019.

MSONKHANO WA MISASA   =      14 OKOTOBALA MPAKA 20 OKOTOBALA 2019.

TSIKU LALIKULU LOMALIZA    =     21 OKOTOBALA 2019.

 

Matsiku oyerawa amayambika  madzulo a tsiku limeneli dzuwa lisanalowe.

MA  ADILESI YA MPINGO WA CONTINUING CHURCH OF GOD.

1036 W. Grand Avenue,

Grover beach,Ca 93433,

U S A.

www.ccog.org

MALAWI  CONTINUING  CHURCH  OF  GOD.

P O BOX 60, MIGOWI,

PHALOMBE,

MALAWI,

Tel : +265 999 046 865,  +265 888 261 344.

Posted in Uncategorized